#Mwanza #Border
Pasqually Zulu Mneneri wa nthambi yowona za anthu olowa ndi kutuluka m'dziko muno pa chipata Cha Mwanza wati boma latumiza ma bus anayi (4) omwe anyamuka dzulo kupita ku South Africa kukatenga mzika za dziko la Malawi zomwe zikuvutikira ku South Africa kamba ka m'bindikiro / lockdown.
.
Ma bus akuyembekezeka kukatenga a Malawi ku Cape Town, Kwazulu Natal ndi Johannesburg ndipo azabwerera kuno ku Malawi kumapeto kwa Sabatayi.
.
Mu nkhani ngati yomweyi, matupi enanso a anthu omwalira omwe ndi mzika za dziko la Malawi okwana 6 afika m'dziko muno ku Mwanza border kuchokera ku South Africa, anthuwo anamwalira ku South Africa pa nthawi ya Lockdown masiku apitawo kunafikanso matupi a anthu okwana 10 kuchokeranso ku South Africa omwe anamwalira pa zifukwa zosiyana siyananso pa nthawi ya Lockdown kupangitsa kuti chiwerengero Cha a Malawi omwalirira ku South Africa chifike pa 16.